Yobu

Chapter 32

1 Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama.

2 Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga.

3 Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa.

4 Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo.

5 Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.

6 Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati: "Ine ndine wamngʼono, inuyo ndinu akuluakulu, nʼchifukwa chake ndimaopa, ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.

7 Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula; anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’

8 Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu, mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.

9 Si okalamba amene ali ndi nzeru, si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.

10 "Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni; inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’

11 Ndadikira nthawi yonseyi, ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula, pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,

12 ineyo ndinakumvetseranidi. Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu; palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.

13 Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru; Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’

14 Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine, ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.

15 "Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso; mawu awathera.

16 Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano, pakuti angoyima phee wopanda yankho?

17 Inenso ndiyankhulapo tsopano; nanenso ndinena zimene ndikudziwa.

18 Pakuti ndili nawo mawu ambiri, ndipo mtima wanga ukundikakamiza;

19 mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo, ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.

20 Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike; ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.

21 Sindidzakondera munthu wina aliyense, kapena kuyankhula zoshashalika,

22 pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika, Mlengi wanga akanandilanga msanga."