Masalimo

Chapter 129

1 "Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga," anene tsono Israeli;

2 "Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane.

3 Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali:

4 Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa."

5 Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi.

6 Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule;

7 sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo.

8 Odutsa pafupi asanene kuti, "Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova."