Masalimo

Chapter 13

1 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?

2 Ndidzalimbana ndi maganizo anga ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti? Mpaka liti adani anga adzandipambana?

3 Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga. Walitsani maso anga kuti ndingafe;

4 mdani wanga adzati, "Ndamugonjetsa," ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.

5 Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika; mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.

6 Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wandichitira zokoma.