Masalimo

Chapter 46

1 Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.

2 Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,

3 ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu, ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.

4 Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu, malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.

5 Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa; Mulungu adzawuthandiza mmawa.

6 Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa; Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.

7 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

8 Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova, chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.

9 Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo; amatentha zishango ndi moto.

10 Iye akuti, "Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu; ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu; ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi."

11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.