Masalimo

Chapter 52

1 Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu? Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse, iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?

2 Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena; lilime lako lili ngati lumo lakuthwa, ntchito yako nʼkunyenga.

3 Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi. Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona. Sela

4 Umakonda mawu onse opweteka, iwe lilime lachinyengo!

5 Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya: iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako; iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.

6 Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha; adzamuseka nʼkumanena kuti,

7 "Pano tsopano pali munthu amene sanayese Mulungu linga lake, koma anakhulupirira chuma chake chambiri nalimbika kuchita zoyipa!"

8 Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu; ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu kwa nthawi za nthawi.

9 Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita; chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.