Masalimo

Chapter 82

1 Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu; Iye akuweruza pakati pa "milungu."

2 "Mudzateteza osalungama mpaka liti, ndi kukondera anthu oyipa?

3 Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.

4 Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

5 "Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse. Amayendayenda mu mdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

6 "Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu, nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’

7 Koma mudzafa ngati anthu wamba; mudzagwa ngati wolamula wina aliyense."

8 Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi, pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.