Masalimo

Chapter 70

1 Fulumirani Mulungu kundipulumutsa; Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.

2 Iwo amene akufunafuna moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene akukhumba chiwonongeko changa abwezedwe mopanda ulemu.

3 Onse amene akunena kwa ine kuti, "Aha, aha," abwerere chifukwa cha manyazi awo.

4 Koma onse amene akufunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, "Mulungu akuzike!"

5 Koma ine ndine wosauka ndi wosowa; bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu. Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga; Inu Yehova musachedwe.