Masalimo

Chapter 30

1 Ndidzakukwezani Yehova, chifukwa mwanditulutsa kwakuya, ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.

2 Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa.

3 Inu Yehova, munanditulutsa ku manda, munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

4 Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika; tamandani dzina lake loyera.

5 Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa.

6 Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, "Sindidzagwedezekanso."

7 Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima.

8 Kwa Inu Yehova ndinayitana; kwa Ambuye ndinapempha chifundo;

9 "Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga ngati nditsikira ku dzenje? Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?

10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; Yehova mukhale thandizo langa."

11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina; munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,

12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.