Masalimo

Chapter 75

1 Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.

2 Mumati, "Ine ndimayika nthawi yoyenera, ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.

3 Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera, ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba. Sela

4 Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.

5 Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba; musayankhule ndi khosi losololoka.’ "

6 Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo kapena ku chipululu.

7 Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.

8 Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse.

9 Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya; ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.

10 Ndidzadula nyanga za onse oyipa koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.